LILONGWE: Wapampando wa gulu la Make Malawi Great Again(MMGA)Dymon Banda, watsutsa zomwe anena a Lyton Mangochi kuti ndiwo omwe atenga utsogoleri wa gululo. Amangochi anena izi mu kanema yemwe iwo atulutsa pa tsamba la mchezo ponena kuti ndiwo omwe atenga utsogoleri wa MMGA kwa mtsogoleri wake Hon. Kamlepo Kalua.A Lyton mangochi ananena kuti Kalua “wasiya gululo” atalengezedwa kukhala CEO wa Umodzi Holdings Limited. Lyton Mangochi. A Banda ati kusankhidwa kwa Kalua kukhudza pang’ono, koma sikunasokoneze ntchito ya MMGA. “Tinakhudzidwa ndi udindo wake watsopano monga CEO, inde. Koma MMGA si bizinesi ya munthu mmodzi. Ili ndi dongosolo labwino ndipo ili ndi komiti yaikulu yomwe ikuyendetsa ntchito zake mokangalika. Tinadabwa kwambiri ndi malingaliro a comrade Mangochi,” adatero Banda. Mtsogoleri yemwe anayambitsa gululo, Hon. Kamlepo Kalua, anavomeleza zomwe anena a Banda. “MMGA ilipo, ikugwira ntchito ndipo ili m’manja mwa komiti yaikulu. Kwatenga nthawi yayitali ndisanalakhulane ndi comrade Mangochi. Sindikudziwa kuti ndinawapatsa bwanji ndipo ndipereka MMGA kwa iwo ngati ndani? Si bizinesi ya munthu mmodzi,” anatero Kalua. kamlepo Kalua: Atsutsa Zomwe anena a mangochi Mangochi mu kanema wawo anadzudzula atsogoleri andale chifukwa chosiya maudindo chifukwa cha “mapwevupwevu” omwe akuluakulu a DPP akusangalala nayo. A Mangochi sanapezeke kuti ayankhepo pa nkhaniyi. MMGA ndi gulu lomwe cholinga chake ndi kuteteza utsogoleri wa dziko, kulimbikitsa ulamuliro wabwino, demokalase ndi ufulu wachibadwidwe. Pakadali pano gulili likutsogozedwa ndi Dymon Banda ndipo Cornelius Lupenga ndi mlembi wa nkhani ndi zofalitsa. Post navigation Leader of Opposition Simplex Chithyola Banda Lashes Out at DPP Government The Shadow of Diplomacy: The Pakistani Businessman Who Wore the Consul’s Mantle in Malawi